Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

ECM Ipempha Akhristu Atenge Mbali Pa Ulendo Wa Ndawala

$
0
0

Mpingo wa katolika mdziko muno molumikizana ndi mpingo wa evangelical wapempha akhristu onse mdziko muno kuti atenge nawo mbali pa ulendo wa ndawala womwe wakonzedwa kuti uchitike pa 6 mwezi wa mawa.

Malinga ndi chikalata chomwe chasayinidwa ndi mlembi wamkulu wa bungwe la ma episkopi a mpingo wa katolika mdziko muno la Episcopal conference of Malawi (ECM),bamboHenry Saindi, cholinga cha ulendo wa ndawala wu ndi chofuna kukakamiza boma kuti lisavomereze lamulo lochotsa pathupi komanso maukwati a amuna kapena akazi okhaokha.

Chikalatachi chati mipingo iwiriyi ndi yokhudzidwa kwambiri ndi anthu amene akumenyera maufuluwa kaamba koti moyo wa munthu ndi woyenera kusamalidwa, kuchengetedwa komanso kutetezedwa kuyambira pamene mwana asanabadwe komanso ukwati wa pakati pa mamuna ndi mkazi ukuyenera kulemekezedwa.

Ulendo wa ndawalawu uchitika mmizinda yonse inayi ya Mzuzu, Lilongwe, Blantyre komanso Zomba. Chikalatachi chatinso izi zichitika m’maboma onse 28 a mdziko muno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875