Apolisi m’boma la Mangochi amanga bambo wina wa zaka 65 zakubadwa kaamba kopezeka ndi mankhwala popanda chilolezo. Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo sergeant Amina Tepani Daudi wati dzulo, apolisi molumikizana ndi a unduna wa za umoyo amafufuza onse omwe akugulitsa mankhwala opanda chilolezo ndipo anapeza bamboyu Levison Mayenda pa msika wa Ntanga m’bomalo akugulitsa mankhwala osiyanasiyana mu shop mwake koma opanda mapepala omuyenereza. Mkuluyu anamangidwa pomwepo ndi kulandidwa mankhwalawo ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu ndi kukayankha mlandu wopezeka akugulitsa mankhwala popanda chilolezo. Apolisi ku Namwera m’boma lomweli la Mangochi amanganso bambo wina wa zaka 31 zakubadwa kaamba kopezeka ndi chamba cholemera ma kilogram 35. Malinga sergeant Daudi, apolisi a pa Roadblock ya Idrus nsewu wa Bakili Muluzi ndi omwe agwira mkuluyi dzulo pamene amafuna kudutsa ndi galimoto lake pa malopa. Mkuluyu anamangidwa pa malo pomwepo ndi kulandidwa chambacho ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu ndi kukayankha mlandu wopezeka ndi chamba zomwe ndi zosemphana ndi gawo 6 la malamulo oyendetsera dziko lino.
↧