Anthu awiri afa, anthu ena atawaotcha ndi moto potsatira ziwawa zomwe anthu m`dziko la Zambia akuchitira anthu obwera (Xenophobia) mu mzinda wa Lusaka.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, anthu m`dziko la Zambiaakuchitira zamtopola mzika za dziko la Rwanda potsatira phekesera yoti mzika za dziko la Rwanda zikumapha anthu ndi kumawadula ziwalo.
Nduna ya za m`dziko, Davis Mwila wati anthu omwe afa ndi mzika za dziko la Zambia.
Apolisi amanga mzika 250 za mdziko la Zambia ndipo sitolo zoposa 60 za mzika za dziko la Rwanda zawotchedwa.
Pakadali pano anthu asanu ndi m`modzi aphedwa ndikuchotsedwa ziwalo m`dziko la Zambia.