Nthambi yoona zolowa ndi kutuluka ya Immigration pa chipata cha Chiponde m’boma la Mangochi yapempha anthu m’dziko muno kuti apewe kukopeka ndi anthu omwe akumabwera m’madera osiyanasiyana ndi kumawuza kuti awatenge ndi cholinga choti akawapezere ntchito zabwino ku madera ena kamba koti ambiri mwa iwo akumakhala ndi zolinga zofuna kuwazembetsa kuti azikawagwiritsa ntchito ngati akapolo kapena kukaphedwa kumene.
Mkulu wa pamalo-wa a Henry David Chidakwa anena izi pa sukulu ya pulayimale yomwe ikupezeka pa chipatachi m’bomalo pa mwambo wa zochitika-chitika zofalitsa mauthenga akuyipa kochitirana nkhanza ndi mchitidwe wogulitsa ndi kuzembetsa anthu umene wakhudzanso dziko lino.
Mabungwe A Norwegian Church Aid , Rights Advice Center,Salvation Army omwe ali pansi pa bungwe lalikulu lolimbana ndi mchitidwe wozembetsa anthu m’dziko muno la Malawi Network Against Human Trafficking ndi omwe anakonza mwambo-wu ngati njira imodzi yotengapo gawo m’masiku16 omwaza mauthenga okhudza kuthetsa nkhanza padziko lonse , omwe anayamba pa 25 mwezi watha pa dziko lonse.
Polankhulanso mkulu wa bungwe laRights Advice Centerm’boma la MangochiaMadalitso Masacheati ndi okondwa kuti bungwe lawo pamodzi ndi mabungwe ena atengapo gawo pa ntchito yomwaza mauthenga okhudza kuthetsa kwa nkhanza m’masiku 16-wa.
Zochitika chitika-chitikazi zinayamba ndi chiwonetsero cha pa nseu Road Show yomwe inayambira m’dera la mfumu yayikulu Jalasi m’boma la Mangochi ndi kukathera pa msika waukulu wa Chipondem’bomali.