Anthu asanu ndi anayi afa ndipo pali chiyembekezo chakuti chiwerengero cha anthuwa chikhoza kukwera potsatira moto wamphamvu omwe unabuka mnyumba ina mdera la Oakland mu mzinda wa California.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC mnyumbayi munali anthu osachepera zana limodzi ndipo malipoti akusonyeza kuti nyumbayi inalibe zipangizo zozimitsira moto.
Padakali pano anthu ochita kafukufuku ati akuchita dongosolo loti achite kafukufuku ngati nyumbayi inamangidwa moyenera potsatira malamulo a zomangamanga.