Akhristu a pa tchalichi laFrancis Chaviyere Woyeraku NamweramuDayosiziya Mangochiati apitiriza kudzipereka pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino monga momwe nkhoswe yawo inali kuchitira.
Wapampando wa komiti yomwe imayendetsa mwambo wa chaka chokondwelera nkhonswe ya ya tchalichili a Sidrick Jangiyaanena izi pa mwambo wa chakachi omwe unachitikaloweruka ku malo a tchalichili.
Malingana ndi a Jangiya chakachi chinayamba ndi mwambo wa msembe ya misa yomwe anatsogolera ndi bambo mfumu a parishi ya Namwera bambo Baziliyo Nsuli.
Polankhulanso wapampando wa tchalichili mayi Ida Shalifapempha akhristu onse a mpingo wakatolika m’dziko muno kuti azikonda kuchita miyambo yokumbukira nkhoswe za matchalichi kapena mayina awo kaamba koti zimathandiza akhristu kuti azikhala olimbika pogwira ntchito zokomera Mulungu monga momwe oyera-wa anali kuchitira m’moyo wa pansi pano.