Sisteri wina wa chipani cha Franciscan mdziko la Congo ati waphedwa mdera la Bakavu pa sukulu yomwe amagwirapo ntchito.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican anthu awiri omwe anatenga mipeni analowa mu ofesi ya Sister Marie Claire ndi kumubaya kangapo konse komanso anaba ndalama zomwe zimagwiritsidwa ntchito pa kayendetsedwe ka sukuluyo zomwe zinali mu ofesiyo.
Padakali pano apolisi ati agwira anthu awiri omwe akuwayimba mlandu wakupha.
Malipoti ati chiwembu cha mtunduwu chinachikanso mmwezi wa May chaka chino pomwe wansembe wina Bambo Vincent Machozi anaphedwa ati kaamba koti amatulutsa zithunzi za anthu omwe amakhudzidwa ndi ziwembu kuphatikizapo anthu ochita ziwembuwo.