Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Njala Ikuyembekezeka Kuchepa M’boma la Chikwawa

$
0
0

Vuto la njala akuti likuyembekezeka kuchepa m’boma la Chikwawa potsatira ndondomeko yabwino ya ulimi wa nthilira imene yakhadzikitsidwa m’bomalo.

Mkulu wowona za ndondomeko za chitukuko m’bomalo a Kelvin Harawa ndi omwe anena izi m’mudzi mwa Mwalija m’dera la mfumu yayikulu Kasisi pomwe bungwe Velt Hunga Hilfe limakhadzikitsa ndondomeko-yi.

A Harawa ati kukhadzikitsidwa kwa ndondomekoyi kuthandiza kuti anthu a m’bomalo azitha kulima ndi kukolora kangapo zomwe zithandizenso kuti bomalo lidzikhala ndi chakudya chokwanira nthawi zonse.

Polankhulanso a Richard Kautale omwe ndi mkulu oyanganira ndondomekoyi m’bungwe la Velt Hunger Hilfe ati bungwe lawo lidzipeleka pothandiza alimiwa kuti apindule koposa ndi ntchito za ulimi m’bomalo .

Maanja 400 ndi amene ali pa m’ndandanda woti apindule ndi ntchito za ulimi m’bomalo.

Bungwe laVelt Hunga Hillfe ligwira ntchito zake ndi thandizo la ndalama zokwanira 1.8 Billion Kwacha kuchokera ku bungwe la European Union(EU).

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>