M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse PAPA FRANCISCO wapempha atsogoleri a amayiko pa dziko lonse kuti alimbikitse ulamuliro wabwino pakati pa anthu omwe akuwatsogolera.
Papa walankhula izi pomwe amapereka uthenga wake wokhudzana ndi tsiku lofalitsa mauthenga akuthetsa kwa mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale komaso lokumbukira za maufulu omwe anthu ali nawo.
Iye wati m’dziko momwe muli ulamuliro wabwino ndiye kuti simumapezekanso m’chitidwe wa ziphuphu ndi katangale kaamba koti zinthu ziwiri-zi zimayendelana.
Mayiko pa dziko lonse agwilizana mawa pochita mwambo wa tsiku lokumbukira za mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale, ndipo loweluka ndi pamene kukhale mwambo wa tsiku loganizira za maufulu a wanthu pa dziko lonse.