Mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse Papa Fransiscowapitiriza kupempha akhristu kuti kubadwa kwa Yesu Khristu kudzabweretse Chilungamo, mtendere komanso chimwemwe mmitima mwawo.
Papa amalankhula izi lero ku likulu la mpingowu ku Vatican pa mwambo omwe amakhala nawo lachitatu lirilonse wocheza komanso kupereka uthenga kwa anthu omwe amasonkhana pa bwalo la St. Peters Square.
Pamepa papa anawerenga mawu ochokera m’buku la Yesaya mutu 52 ndime ya 7 omwe akukamba za kukongola kwa mapiri zomwe akuti akhristu akuyenera kukhalanso okongola m’mitima mwawo kuti mpulumutsi adzabadwire malo oyera.