Ophunzira a sukulu ya pulaimale ya Nthumbi m’boma la Ntcheu anayenda ulendo wa ndawala posonyeza kusakondwa ndi kudula mitengo mwa chisawawa komwe kukuchitika m’madera ozungulira sukuluyo.
Polankhula pamapeto wa uledowo womwe unali wa pafupifupi ma kilometer khumi wapampando wa bungwe loona za chilengedwe pa sukuluyi yemwenso ndi ophunzira wa Std 8, Henderson Dagalasi anati anaganiza zochita izi atawona kuti anthu okhala midzi yozungulira sukuluyo akuthandizira kuwonongeka kwa chilengedwe podula mitengo yowotchera makala.
Iye anati pali chiopsezo kuti ngati anthu apitilira kuchita izi ndiye kuti anthu mtsogolomu azavutika.
Polankhula ndi atolankhani a MANA group village head Champiti amenenso anayenda nawo ulendo wa ndawalawu anayamikira ophunzirawa kaamba kotengapo mbali maka polankhulapo mbali yawo pa nkhani zosamalira za chilengedwe.