Ophunziraa msukulu za pulaimale m’boma la Salima adandaula kaamba ka makhalidwe a aphunzitsi ena omwe ati akukolezera kuti ana aakazi azisiyira sukulu panjira.
Ophunzirawa anena izi pa sukulu ya Msalura Community Day Secondary pa mwambo womwe unakonzedwa ndi arkidayosizi ya mpingo wa katolika ya Lilongwe komanso bungwe la FAWEMA ndi cholinga cholimbikitsa ana aakazi kusalekera sukulu panjira yomwe akuitcha Keeping Girls In School (KGIS).
Ophunzirawa anena izi kudzera mu njira zosiyanasiyana monga sewero, nyimbo, magule, ndakatulo komanso maumboni omwe atsikana ena anapereka omwe amasonyeza kuti aphunzitsi aamuna ambiri ndi omwe akukhudzidwa ndi mchitidwe womawopsyeza komanso kugona ndi atsikanawa.
Polankhula ndi atolankhani a Malawi News Agency (MANA), mkulu woyang’anira sukuluzi a Nyson January Chisi anati ofesi yawo imapereka chilango chokhwima kwa mphunzitsi wopezeka akuchita makhalidwe oyipawa.
Polankhulapo m’modzi mwa akuluakulu ku unduna wa zamaphunziro mdziko muno a Albert Saka anathokoza boma komanso mabungwe osiyanasiyana kaamba kotenga gawo lalikulu loonetsetsa kuti atsikana mdziko muno aphunzire bwino.