Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akazembe a m’maiko kuti awonenetsetse kuti akudzetsa mtendere popewa za mtopola mu ulamuliro wao.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa amalankhula izi ku likulu la mpingowu ndi akazembe a mmaiko a Burundi, Fiji, Mauritius, Moldova, Sweden, ndi Tunisia omwe amakapereka kalata zowayenereza kukhala ku likulu la mpingowu ngati akazembe.
Papa anauza akazembewa kuti agwilire ntchito limodzi pothetsa za mtopola zomwe zikuchitika mmaiko osiyanasiyana.
Papa anankhula ndi akazembewa potsatira uthenga wa tsiku loganizira za mtendere lomwe ndi pa 1 January lomwe mutu wake ndi “Kuthetsa Zamtopola, Njira Ya Ndale Za Mtendere.”