Bwalo lamilandu mdziko la South Africa lati ganizo lothetsa milandu 7 hundred 83 ya katangale ya pulezidenti wa dzikolo Jacob Zuma likuyenera kuwunikidwanso.
Malipoti a wailesi ya BBC ati milanduyi inathetsedwa chisankho cha pulezidenti cha mchaka cha 2009 chomwe pulezidenti Zuma adapambana chitatsala ndi sabata zochepa kuti chichitike.
Malinga ndi mmodzi mwa oweruza milandu ku bwaloli a Audrey Ledwaba ganizoli lomwe linachokera kwa mkulu oyimilira milandu ku mbali ya boma silinali loyenera ngakhale pulezidenti Zuma amakana za milanduyi kuti iye sakudziwapo kanthu.