Mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wasintha ena mwa ma udindo a m’boma potsatira mphamvu zomwe ali nazo kuchokera mmalamulo oyendetsera dziko lino.
Malinga ndi chikalata chomwe chasainidwa ndi mneneri wa kunyumba ya boma Mgeme Kalilani a Nicholus Dausi ndi nduna ya zofalitsa nkhani komanso mneneri wa boma omwe alowa m’malo mwa m’busa Malisoni Ndau amene tsopano si nduna ya boma.
Pulezidenti yu wasankhanso a Lloyd Muharakukhala mlembi wamkulu wa boma ndipo a George Mkondiwa awasankha kukhala kazembe wa dziko lino ku dziko la India ndipo yemwe anali kazembe wa dziko lino mdziko la India Dr. Isaac Munlo amusankha kukhala mkulu mu unduna woona zamgwirizano pakati pa dziko lino ndi maiko ena.
Chikalatachi chati maudindowa ayamba kugwira ntchito yake lero pa 19 December 2016.