Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Zigawenga za Islamic State Zavomera Kuti Zachita Chiwembu Mdziko la Turkey

$
0
0

Zigawenga za chisilamu za Islamic State ati ndi zomwe zachita chiwembu chomwe chaphetsa anthu 39 ndi kuvulaza ena pa malo ena achisangalalo mu mzinda wa Istanbul mdziko la Turkey.

Zigawengazi ati zavomera za chiwembuchi kudzera mu uthenga omwe zatulutsa ndipo kuti zinachita izi kaamba koti anthu ambiri a chipembedzo cha chisilamu akhala akuphedwa mdziko la Syria potsatira mabomba ochokera mu ndege za mlengalenga zochokera mdziko la Turkey.

Malipoti a wailesi ya BBC ati kumalowa kunafika munthu wina yemwe uthengawu wafotokoza kuti ndi m’modzi mwa zigawengazi ndipo ati anakwanitsa kupha komanso kuvulaza anthu omwe anali pa malowa powaombera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>