Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Adzudzula Mchitidwe wa Chiwembu Mdziko la Turkey

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco, wadzudzula mchitidwe wa chiwembu omwe wachitika mdziko la Turkey pomwe anthu 39 aphedwa ndipo ena 69 avulala pa malo ena achisangalo mu mzinda wa Instanbul mdzikolo.

Polankhula ndi alendo omwe anafika ku likulu la mpingowu pa bwalo la St. Peters, Papa wati awayikiza m’mapemphero anthu omwe akhudzidwa pa chiwembuchi ngakhalenso mabanja awo.

Pamenepa Papa wati apempha Mulungu kuti atsogolere anthu onse omwe akukumana ndi mavuto monga zamtopola mmaiko awo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC izi zachitika m’bandakucha wa lero pomwe anthuwa anali pa malo ena a chisangalalo poyembekezera kulowa mu chaka  chatsopano cha 2017.

Malipoti ati kumalowa kunafika munthu wina wosadziwika yemwe anali ndi mfuti  ndipo ati anakwanitsa kuombera ndikupha komanso kuvulaza anthu omwe anali pa malowa.

Padakali pano mtsogoleri wadzikolo watsimikizira atolankhani mdzikomo kuti apolisi achita chotheka kufufuza za anthu omwe akuchita zamtopola za mtunduwu ati kaamba koti aka sikoyamba kuti chiwembu cha mtunduwu chichitike mdzikolo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>