Apolisi a pa nsewu mdziko muno adandaula kaamba ka kuchuluka kwa ngozi za pansewu m’boma la Mangochi.
Mkulu wa apolisi a pansewu mdziko muno Assistant Commissioner Mcferson Matowe wauza Radio Maria Malawi kuti ngozi za pansewu zikuchulukira m’boma la Mangochi kuposa maboma ena onse mdziko muno kaamba ka galimoto za matola.
Malinga ndi a Matowe m’chaka cha 2016 anthu amene afa pa ngozi za pa nsewu m’boma la Mangochi ndi okwana 68.
“Anthu amene afa pa ngozi za pansewu chifukwa chkwera galimoto za matola ndi 68 m’boma la mangochi lokha koma ovulala ndiye ndi osaneneka. Vuto lalikulu ndi kusowa umwini wa anthu okwerawo komanso eni ake a galimoto za lorry akukonda ndalama osati miyoyo ya anthu amene akuwatenga,” anatero Assistant Commissioner Matowe.
Pamenepa iwo ati apolisi ayesetsa kuphunzitsa anthu kuti adziwe kuyipa kokwera galimoto za matola komanso azipereka chilango kwa onse onyamula anthu mu galimoto za mtundu wa Lorry.
“M’madera ambiri zmenezi zinatha kwatsalira ndi ku mangochi kokha koma tiyesetsa kuphunzitsa anthu kupewa ngozi za mtunduwu komanso padakali pano munthu akapezeka ndi mlandu woyika miyoyo ya anthu pa chiopsezo potenga anthu mgalimoto ya matola azikakhala ku ndende zaka zoposera zisanu komanso ena padakali pano tikumawalipilitsa ndalama zokwana 200,000 kwacha,” anatero a Matowe.