Quantcast
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mipingo ndi zipembedzo zakhazikitsa ndondomeko yothandiza kuti zisankho zidzayende bwino

Magulu azipembedzo zosiyanasiyana  mdziko muno atsekulira ntchito yomwe akuyitcha Interfaith Elections Initiative ngati njira imodzi yothandizira kuti zisankho za chaka cha mawa zidzayende bwino.

Zolinga zantchito yomwe yakhazikitsidwayi ndikufuna kuwonetsetsa kuti zisankho za mchaka cha mawa zidzakhale zovomerezeka,  zidzakhale zomwe amayi ambiri atenge nawo mbali, kulimbikitsa mgirizano pakati pa azipembezo ndiponso kuonetsetsa kuti anthu akukavota momvetsetsa pankhani zachisankho. Ntchitoyi yatsekuliridwa mu nzinda wa Lilongwe ndipo ikuyembekezeka kugwiridwa m’maboma 20 a mdziko muno ndi mabungwe 15 a Chikhristu ndiponso 5 a Chisilamu. Polankhula potsekulira mwambowu mlembi wamkulu ku offesi ya ma Episikopi ampingo wa Katolika , Bambo George Buleya ati zisankho zimakhala zovomerezeka ngati zikusonyeza chifuniro cha Mulungu.

“iyi ndi mbali imodzi ya udindo wa akuluakulu  azipembezo pothandiza anthu kuti achite zisankho zoyenera pomwe akuyembekezereka kukavota chaka cha mawa”. Anatero Bambo Buleya.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>