Apolisi mdziko la Turkey ati amanga anthu angapo omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi chiwembu chomwe chinaphetsa anthu 39 pa malo ena achisangalalo mdzikolo.
Malipoti a wailesi ya BBCati anthu omwe awagwirawa ndi ochokera mdziko la China ndipo padakali pano apolisi akuchitabe kafukufuku pofuna kupeza munthu yemwe anachita chiwembuchi.
Gulu la zigawenga la chisilamu la Islamic State ISati linavomera za chiwembuchi kudzera mu uthenga omwe linatulutsa ndipo kuti zinachita izi kaamba koti anthu ambiri a chipembedzo cha chisilamu akhala akuphedwa mdziko la Syria potsatira mabomba ochokera mu mlengalenga ku ndege za asilikali a mdziko la Turkey.