Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wapereka sacrament la ubatizo kwa ana okwana 28 pa nsembe ya misa yomwe inachitikira mu tchalitchi la Sistine.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, Papa anaperekanso uthenga womwe umaperekedwa pa tsiku la ubatizo kwa ana komanso makolo.
Iye anati chikhulupiliro si kungonena pemphero la kumvera pa tsiku la mulungu lokha koma kukhulupilira mu choona, mwa mulungu komanso kuphunzitsa ena kudzera mu zitsanzo za m’moyo wathu.
Mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu anati chikhulupiliro ndi kuwala komwe kumakula muntima mwa munthu ndi chifukwa chake munthu akamabatizidwa amalandira kandulo yemwe amathandiza kuti aziwona zinthu zosiyanasiyana.
Pamenepa papa anapempha makolo a anawa kuti atenge gawo lalikulu lothandiza anawa kuti akulitse chikhulupiliro chawo mwa Yesu Khristu.