Mtsogoleri wa dziko la Iran a Ayatollah Ali watsogolera anthu mdzikolo kukhudza imfa ya mtsogoleri wopuma wa dzikolo a Akbar Hashem Rafsanjani omwe amwalira ali ndi zaka 82.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, mtsogoleri opumayu wamwalira lamulungu usiku pa chipatala china mu mzinda wa Tehran atadwala nthenda ya mtima.
Malipoti ati kupatula kusemphana kwawo mu zina, mtsogoleriyu wati dziko la Iran lataya munthu wofunikira kwambiri ku dzikolo komanso ku chipembedzo cha chisilamu.
Pakadali pano boma la dzikolo lalengeza kuti pakhale masiku atatu okhudza imfayi ndipo lachiwiri, tsiku lomwe akayike m’manda thupi la malemuwa mu mzinda wa Tehran likhala tsiku la tchuthi.
A Rafsanjani analamulira dzikolo kuyambira mchaka cha 1989 mpaka 1997.