Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Engineer Wazipha Pozimangilira

$
0
0

Bambo wina yemwe amagwira ntchito ngati engineer ku bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe wazipha pozimangilira ku denga la nyumba yake.

Malinga ndi wofalitsa nkhani za polisi pa bwalo la ndegeli Sergeant Sapulain Chitonde, bamboyu Dennis Chauluka wa zaka 33 zakubadwa yemwe anali ndi mbiri ya nthenda ya khunyu anapezeka lachiwiri atazimangilira ku denga kwa nyumba yake, thupi lake litawonongeka ndipo sanasiye uthenga uli wonse wokhudza imfa yake.

Mkuluyu ati pa nthawiyi anali atamaliza maphunziro ake ndipo amayembekezeka kutumizidwa kukagwira ntchito ku bwalo la ndege la Mzuzu.

Malinga ndi yemwe amakhala moyandikana ndi mkuluyu ati anamuona mkuluyu kotsiriza pa 7 mwezi uno.

Zotsatira za chipatala cha Lumbadzi zasonyeza kuti mkulkuyu wafa kaamba kobanika kaamba kozimangilira. Dennis Chaulukaamachokera m’mudzi mwa Ndaone mfumu yaikulu Nsabwe m’boma la Thyolo ndipo wasiya mkazi ndi mwana m’modzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>