Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dr. Chaponda Alamulidwa Kuti Ayime Kaye pa Unduna

$
0
0

Bwalo lalikulu la milandu mu mzinda wa Mzuzu lagamula kuti nduna ya za ulimi chitukuko cha madzi ndi nthilira Dr. George Chaponda ayime kaye pa udindowu kufikira zofufuza zokhudza chimanga chomwe boma linagula mdziko la Zambia zitatha.

Mneneri wa mabwalo a milandu mdziko muno a Mlenga Mvula atsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi ndipo ati izi zadza potsatira madandaulo omwe mabungwe komanso anthu ena anapereka ku bwaloli kuti ndunayi iyambe yayima kaye pa udindowu ndi cholinga chopereka mpata ku zofufuza zokhudza nkhaniyi zomwe zili mkati.

AKalekeni Kaphale ndi mlangizi wa boma pa nkhani za malamulo ndipo ati akatenga chiletso pa chigamulochi. Polankhulapo m’modzi mwa akatswiri pa nkhani za malamulo mdziko muno a Benedicto Kondowe ati chigamulochi chasonyezeratu poyera kuti malamulo adziko lino akugwira bwino ntchito yake.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>