Chipatala cha Kalembo m'boma la Balaka ati chikusowa malo owonjezelera chipatachi kaamba koti anthu ena analowelera malo a chipatalachi.
Dotolo wamkulu pa chipatalachi Patricia Tembo wauza Radio Maria Malawi kuti zitukuko zambiri zakhala zikulephereka kaamba ka kusowa kwa malo ndipo ati anthu amene akuwaganizira kuti analowelera malo a chipatalawa akufuna chipukuta msonzi kuti apereke malowo ku chipatalacho.
Mayi Tembo ati mwazina chipatalachi amafunitsitsa chikanakhala mu mpanda kuti malire adziwike bwino komanso ngati kupereka ulemu kwa amayi amene amachilira pa chipatalachi.
Polankhulapo mkulu woyang'anira madotolo ku ofesi ya za umoyo m’bomali Dr. Leonard Chafewa anavomereza za vutoli koma anati ofesi yawo ikuyesetsa ndipo vutoli lithetsedwa posachedwapa.