Kazembe wa dziko la Australia wayamikira mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco kaamba ka mawu a mphamvu okhudza kudzetsa mtendere komanso kuteteza anthu othawa kwawo.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati kazembeyu amathilirapo ndemanga pa mawu amene analankhula papa Francisco lolemba lathali pocheza ndi a kazembe a maiko osiyanasiyana ku Vatican.
Iye wati dziko la Australia lamvetsetsa ndipo walonjeza kuti dzikolo ligwira ntchito limodzi ndi likulu la mpingo wa katolikali pothetsa mchitidwe wozembetsa anthu komanso kuwonetsetsa kuti amayi ndi ana akukhala ndi umoyo wabwino.
Kazembeyu wati mawu a papa Francisco anali a mphamvu komanso opatsa chiyembekezo maka podzetsa mtendere, chitetezo komanso kwa anthu othawa kwawo.