Bungwe la eni minibus m’dziko muno laMinibus Owners Association of Malawi (MOAM) lati ndilokhumudwa kuti anthu okwera ndi amene akuthandizira kuti ma minibus m’dziko muno azinyamula anthu mopyola muyeso.
Bungweli lanena izi posatila ganizo laboma lofuna kuyamba kuyimitsa mtundu wa ma minibus za Vanneti komanso Bongo kuyenda pa msewu m’dziko muno ati ponena kuti galimotozi ndi zimene zikukolezera ngozi zambiri za pamsewu m’dziko muno.
“Ife tinawauza kuti solution sikuletsa ma vanneti kuyenda pansewu chifukwa galimoto zinanso ngati ma bus, ma lorry zimapezekanso zikunyamula anthu ochuluka kuposa mulingo wake. Inde vaneti ndiyaingono koma asaziletse kuyenda pansewu mwina dziko lingopanga malamulo ena okhuza zimenezi,” anatero a Kamange.
Iwo ati akanakonda boma likanakhazikitsa kuti woyendetsa amene apezeke atanyamula anthu ochuluka kupyola muyeso wake azimulanda chiphaso choyendetsera galimoto ndipo akapezeka atachita zimenezi kangapo azimuimitsa kuyenda pa nsewu kwa chaka.