Akhristu a mpingo wakatolika m’dziko muno awapempha akuti adzipeleke pa ntchito yosamalira seminale yayikulu ya St. Peters yomwe ili mu Dayosizi ya Zomba.
Mkulu woyendetsa ntchito za seminalyi bambo Samuel Malamulo anena izi pa mwambo wodzodza madikoni 13 ochokera m’ma dayosizi osiyanasiyana.
Bambo Malamulo ati seminale ya St. Peters ili pa mavuto a akulu a za chuma kotero akhristu eni ake akuyenera kudzipeleka pa ntchito zoyendetsa seminale-yi, kuti ipitilire kudzipeleka pa ntchito yosula amsembe mu mpingowu.
Polankhulanso ku mwambowo episkopi wa dayosizi ya ZombaambuyeGeorge Desmond Tambalaanayamikira ansembe ndi makolo kamba ka chidwi chomwe akhala akuonetsa pothandiza asemino omwe adzodzedwa kukhala ma dikoni-wo.
A Dikoni omwe adzodzedwa-wa ndi ochokera m’ma dayosizi asanu ndi imodzi (6),mwa ma dayosizi asanu ndi atatu (8) amene ali dziko muno.
Mwa madikoni-wa, atatu ndi ochokera mu arkidayosizi ya Lilongwe, m’modzi wochokera ku Zomba, awiri ku Mangochi. Ku Chikwawa kwachokera madikoni atatu, ku Dedza awiri, ndipo ku Blantyre kwachoka awirinso.