Mpingo wakatolika mu arch-dayosizi ya Lilongwe walimbikitsa ana mu mpingo-wu kuti apitirize kudzipereka pa nkhani zakusamilira chilengedwe pofuna kuthana ndi mavuto omwe akudza kaamba kakusintha kwa nyengo.
Arkepisikopi arch-dayosizi-yi olemekezeka ambuye Tarcizius Ziyaye ndi omwe anena izi pakutha pa mwambo wa padera wa chaka cha utumiki wana chomwe chachitika lero ku St Patricks Parish mu arch-dayosizi-yi. Iwo ati yakusintha kwa nyengo ikukhudza wina aliyense kuyambira ana mpaka akuluakulu.
Mmawu ake wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulosi Chilimaomwe anali mlendo wolemekeza pa mwambowo anayamikira mpingo wakatolika polimbikitsa ana kuti azikhala achifundo komanso olimbikira pogwira ntchito makamaka pa nkhani yokhudza kusamala zachilenegedwe.
Mutu wa chaka chakachi unali woti lolani ana abwere kwa ine musawaletse ndipondi mutu umene mpingowu umatsatira pa dziko lonse.
Kumwambowu kunafika ana ochokera m’madinale onse opezeka mu arch-dayosiziyo ndipo mwapadera zochitika zonse za kumwambowu anatsogolera ndi ana.