Wapolisi m’boma laNkhatabay wafa atamwa mankhwala azitsamba omwe sing’anga wina anamupatsa kuti achire ku matenda a m’mimba omwe amadwala.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomaloSergeantIgnasio Essauwatsimikiza za nkhaniyi ndipo wati malemuyu ndiFriday Kalonjerayemwe amagwira ntchito pa polisi yaNkhatabay.
SergeantEssauwati thupi la malemuyu alitumiza kuchipatala kuti akalipime pamene sing’angayu amene amatchuka ndi dzina lotiMfitizalimbaamutsekera mu chitokosi kudikira zotsatira za chipatala pa imfayi.