Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Apepesa Okhudzidwa pa Ngozi ya Ndege Mdziko la Hong-Kong

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonsePapa Franciscowapereka uthenga wa chipepeso kwa anthu amene akhudzidwa pa ngozi ya ndege yomwe yagwa mu mzinda waKyrgyzstanmdziko laHong-Kong.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati ndegeyi yomwe ndi ya mdziko la Turkey imachoka mdziko la Hong-Kong ndipo imayembekezeka kutera pa bwalo la ndege la Manas isanapitilire ku Instabulmdziko laTurkey.

Malinga ndi chikalata chomwe chasainidwa ndi mlembi wamkulu ku Vatican, Cardinal Pietro Parolin, mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu ndi okhudzidwa kwambiri ndi ngoziyi ndipo wapepesa onse omwe ataya okondedwa awo pa ngoziyi makamaka a mdera la Manas.

Papa wati ndi pemphero lake kuti mizimu ya anthu amene afa pa ngoziyi ilandilidwe mchifundo cha Ambuye ndipo wapemphera kuti ntchito yofufuza anthuwa iyende bwino.

Anthu pafupifupi 37 ndi omwe afa pa ngoziyi omwe ambiri ndi a m’mudzi wa Manas.

Pafupifupi theka la nyumba za m’mudzi omwe ndegeyi inagwera pafupi ndi bwalo la ndege la Manas zawonongeka pa ngoziyi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>