Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco ati wapereka uthenga wa chipepeso kwa anthu onse omwe ataya abale awo komanso omwe akhudzidwa pa ngozi ya moto wachilengedwe mchigawo chapakati cha dziko la Chile.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa wapereka uthengawu kudzera kwa mlembi wamkulu wa ku likulu la mpingo wakatolikali Cardinal Pietro Parolin.
Cardinal Parolin wati Papa ayikiza mizimu ya anthu omwe amwalira pa ngoziyi mmapemphero komanso kulimbikitsa abale awo.
Papa wati kudzera mu ngoziyi anthu akuyenera kumanga umodzi pofuna kugonjetsa mavuto omwe akukumana nawo pa nthawiyi.
Malipoti a wailesi ya BBC ati anthu asanu ndi mmodzi 6 afa ndipo ena omwe chiwerengero chake sichikudziwika avulala pa ngoziyi.
Padakali pano anthu oposera 4 sauzande ati achoka mnyumba zawo kamba ka motowu.