Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Ayamikira Ziwonetsero Zoteteza Moyo Mdziko La America

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wayamikira onse omwe anatenga nawo mbali pa ulendo wa ndawala woteteza ufulu wa moyo womwe wachitika dzulo lachisanu mu mzinda wa WashingtonDC mdziko la America.

Malinga ndi uthenga womwe watumizidwa ndi mlembi wamkulu wa ku Vatican Cardinal Pietro Parolin, Papa Francisco akukhulupilira kuti ulendo wa ndawalawu  umene walankhulira ena omwe sangathe kulankhula uthandiza kuteteza ufulu wa moyo.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati chaka ndi chaka anthu zikwizikwi amatenga nawo mbali pa ulendo wa ndawalawu  ndi cholinga chofuna kuteteza ana omwe sanabadwe, kuthetsa kupha anthu popanda zifukwa zenizeni komanso kulimbikitsa maufulu ena okhudza moyo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>