Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dr. Kumpalume Achenjeza Anthu Ochita Chinyengo Mzipatala za Boma

$
0
0

Unduna wa zaumoyo wati uthana ndi anthu onse ochita zachinyengo mu ntchito ya zaumoyo mdziko muno.

Nduna mu undunawu Dr. Peter Kumpalume ndi omwe anena izi pa mwambo omwe bungwe la Clinton Health Association Initiative (CHAI) limapereka katundu osiyanasiyana ku sukulu ya mpingo wa katolika yosula anamwino ndi azamba ya St. Joseph ku Nguludi m’boma la Chiradzulu.

Pamene imathokoza kaamba ka thandizoli, ndunayi yati ndi zokhumudwitsa kuti anthu ena ogwira ntchito mzipatala za boma akumafunsa anthu kulipira pa thandizo  la chipatala lomwe amayenera kulandira mwa ulere.

Polankhulapo m’malo mwa episkopi wa arkidayosizi ya Blantyre, Monsignor Boniface Tamani anayamikira bungwe la CHAI kaamba kokhala ndi chidwi chothandiza ntchito za umoyo pothandiza sukulu ya St. Joseph.

 Iwo ati izi zithandiza kupititsa patsogolo masomphenya a mpingo ofuna kutukula anthu mu magawo onse makamaka mu ntchito za umoyo.

Bungwe la Clinton Health Association Initiative (CHAI) ndi thandizo la ndalama kuchokera ku dziko la Norway likuthandiza sukulu ndi zipatala zomwe zili pansi pa Christian Health Association of Malawi (CHAM) mu njira zosiyanasiyana ndipo yathandiza sukulu yosula anamwino ndi azamba ya St. Joseph pomanga midadada inayi yogona ophunzira, nyumba yochitiramo maphunziro ndi misonkhano komanso kupereka galimoto la mtundu wa Coaster ku sukulu-yi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>