Bungwe la CADECOM mu dayosizi ya Zombalati liwonetsetsa kuti anthu mu dayosiziyo akukhala ndi chakudya chokwanira ngakhale nyengo ikusintha.
Mkulu wa bungwe la CADECOM mu dayosizi yo bambo Patrick Kamba ndi omwe anena izi pa mwambo wokhazikitsa ntchito yobzala mitengo womwe unachitikira mmudzi mwa Massi mfumu yaikulu Mkula m’boma la Machinga.
Iwo ati kudula mitengo ndi imodzi mwa njira zomwe zikudzetsa kusintha kwa nyengo zomwe zikuchititsa kuti anthu asamakhale ndi chakudya chokwanira.
Polankhulapo mkulu woona za nkhalango m’boma la Machinga a Paul Muhosha ayamikira bungwe la CADECOM kaamba kothandiza kubwezeretsa chilengedwe m’bomalo.