Mtsogoleri wa dziko la America Donald Trump wati ganizo lake loletsa nzika zina zochokera ku mayiko ena achisilamu kulowa mdzikolo sikukutanthauza kuti akudana ndi chipembedzo chachisilamu.
A Trump alankhula izi pomwe mzika zina za mdziko la America komanso mayiko ena akhala akuchita ziwonetsero zosagwilizana ndi ganizo la boma la America-lo.
Iwo ati dziko la America limasangalala ndi anthu a m’mayiko ena ndipo lipitiliza kuwalemekeza komabe kwinaku likuteteza mzika zake ku malire a dzikolo.
Anthu mazanamazana akhala akuchita ziwonetsero m’mizinda ya dzikolo posagwilizana ndi ganizolo ndipo ambiri akudandaula kuti dzikolo likuchita tsankho.