Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko la Indonesia a Jusuf Kalla wati ndondomeko yomwe dziko la America lokonza poletsa anthu ochokera ku Mayiko a chisilamu kulowa mdziko la America, kukupereka chikayiko pa m’mene dzikolo likuwaganizira asilamu.
A Kalla ati ndondomekoyo silingakhudze kwambiri dziko lawo koma likupereka chikayiko pa m’mene dziko la America likuganizira asilamu.
Dziko la Indonesia ndi limodzi mwa mayiko omwe kuli asilamu ambiri koma silili pa m’ndandanda wa mayiko omwe anthu ake awaletsa kulowa mdziko la America.
A Donald Trump alamula kuti anthu ochokera m’mayiko achisilamu monga Syria, Iran, IRAQ, Libia, komaso Sudan asamalowe mdziko la America.