Apolisi m’boma la Karonga ati akusunga mchitokosi msilikali wina wa ku Cobbe barracks ku Zomba kaamba komuganizira kuti amalandira ndalama zokwana 80 sauzande kwacha kwa anthu a mmidzi ina ya m’bomalo ndi cholinga choti awapezere ntchito ya usilikali anthuwo.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Constable Davie Mulewa wauza Radio Maria Malawi kuti msilikaliyu Loti Mwakisulu wa zaka 27 zakubadwa wa mmudzi mwa Mwakisulu kwa mfumu yaikulu Kilupula m’bomalo wakhala akuchita izi kuyambira chaka chatha kwa anthu omwe anamaliza sukulu yao kufika fomu 4.
Iwo ati apolisi akhala akumva za mphekesera ya mchitidwewu kufikira dzulo pomwe anatsinidwa khutu ndi anthu a mmudzi wa Mwakawoko m’bomalo komwe msilikaliyu anafika pa nthawiyo.