Apolisi m’dziko la New Guinea akuwaganizira kuti apha ophunzira anayi a pa sukulu ina ya ukachenjede omwe amachita chionetsero chosonyeza kusakondwa ndi zochita za nduna yaikulu ya dzikolo.
Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC chionetserocho chinayambira ku sukulu yawo ndipo chinakathera ku nyumba yamalamulo ya dzikolo.
Ophunzira-wa ati akufuna kuti ndunayi itule pansi udindo wake kuti ikayankhe milandu ya ziphuphu ndi katangale.
Malipoti ati ndunayi ikukana kutula pansi udindo wake ndipo yati sikudziwapo kanthu pa nkhanizi.