Nthambi ya zachilungamo mdziko la America yati ikugwirizana ndi zomwe mtsogoleri wa dzikolo, Donald Trump wachita poletsa anthu a m’maiko ena a chisilamu kolowa mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, nthambiyi yati presidentiyu wachita izi kudzera mu mphamvu zomwe amapatsidwa kuchokera m’malamulo oyendetsera dzikolo ndipo apempha bwalo lalikulu la milandu mdzikolo kuti lamuloli liyambe kugwira lipitilire kugwira ntchito poganizira chitetezo cha dzikolo.
Lamuloli likuletsa anthu othawa kwawo komanso alendo ochokera m’maiko asanu ndi awiri omwe ndi a chipembedzo cha chisilamu kulowa mdziko la America.
Bwalo lalikulu la milandu la dzikolo likuyembekezeka kupereka chigamulo chake lero kuti lamuloli lipitilire kugwira ntchito kapena ayi.
Pakadali pano anthu a m’maiko asanu ndi awiriwa 7, Iraq, Iran, Libya, Somalia, Sudan, Syria komanso Yemen omwe ali ndi zitupa zoyenera akupitilirabe kulowa mdzikolo.