Mayi wina wa zaka 52 zakubadwa wafa atawombedwa ndi galimoto m’boma la Mangochi.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Amina Tepani Daudi wauza Radio Maria Malawi kuti mayiyu Martha Kuswenje anawombedwa ndi galimoto ya mtundu wa Rav4 nambala yake BT 9292 yomwe imayendetsedwa ndi a Ganet Fologonya a zaka 51 a m’mudzi mwa James mfumu yaikulu Kuntaja m’boma la Blantyre.
Sergeant Daudi ati galimotoli lomwe limalowera ku Namwera linali pa liwiro lamphamvu ndipo litafika pa round about ya pa St. Augustine Mangochi Cathedral dalaivala analephera kuwongolera bwino ndipo inaphonya nsewu ndi kugubuduka kangapo ndi kukawomba mayiyu yemwe amayenda m’mbali mwa nsewuwu. Mayiyu ati anavulala kwambiri ndi kufera pomwepo.
Pakadali pano apolisi m’bomali achenjeza anthu kuti azitsatira malamulo a pansewu kuti apewe ngozi za mtunduwu.
Mayi Martha Kuswenje amachokera m’mudzi mwa Chipalamawamba mfumu yaikulu Mponda mboma lomwelo la Mangochi.