Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kanyongolo Wapempha Boma Libwezeretse Maubale Ndi Maiko Ena

$
0
0

Katswiri wa malamulo yemwenso ndi mphunzitsi wa malamulo pa sukulu ya ukachenjende ya Chancellor, Professor Edge Kanyongolo wapempha boma  kuti libwezeretse ubale womwe unasokonekera pakati pa boma la Malawi ndi mayiko komanso mabungwe omwe amathandiza  dziko lino pa chuma.

Professor Kanyongolo wanena izi lachinayi poyankhula  ndi Radio Maria Malawi .

Iwo ati ndondomeko yachuma yachaka chino ipweteketsa anthu osauka chifukwa adzidulidwa nsonkho akagula katundu  wina aliyense.

A Kanyongolo ati dziko la Malawi silinafike podzidalira palokha pachuma chifukwa lilibe zinthu zoziyenereza monga migodi ndi makampani akulu akulu. Iwo ati dziko la Malawi limadalira fodya yekha pa chuma yemwenso sakuyenda bwino pa msika.

Kaswiri wa malamulo-yi wati boma liyenera kuvomereza kuti zinthu mdziko muno sidzilibwino pa chuma. Iwo ati zipatala za mdziko muno muli mavuto ambiri  monga kusowa mankhwala komanso kuchepa kwa ogwira ntchito ndipo wati izi zikusonyeza kuti boma lili pa mpanipani wosonyeza kuti lilibe chuma choyendetsera dziko.

Pa nkhani ya njala yomwe ili m’dziko muno Professor Kanyongolo wapempha boma kuti ligule chimanga chambiri kuti chizakwanire anthu onse omwe alibe chokudya. Iwo ati boma lisadzalowetse ndale podzagawa chimangachi koma chidzafikire aliyense.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>