Bambo wina wafa m’phenzi itamuomba m’boma la Dowa.
Malingana ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo SergeantRichard Kaponda, bambo-yu ndi Dalitso Jose yemwe anali wa zaka 38zakubadwa ndipo amachokera m’mudzi mwa Gomam’dera la mfumu yayikulu Msakambewa m’bomalo .
SergeantKapondaati ngozi-yi inachitikira m’mudzi mwa Gunda m’bomalo.
Iwo ati adakalipano mwana wa malemu-wa Lustia amugonekanso pa chipatala china m’bomalo atakhudzidwanso ndi ngozi-yi pa tsikuli.
Ofalitsa nkhani za apolisiyu wati mphenzi-yi inaomba ndi kupha bambo-yu ali m’nyumba kubisala mvula yamphamvu yomwe imagwa ku delaro.