Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trump Akulingalira Zosintha Pang’ono Lamulo Loletsa Mzika za Maiko a Chisilamu

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la America Donald Trump wati ali ndi malingaliro ongofuna kusintha pang’ono ganizo lake loletsa nzika za mayiko ena achisilamu kulowa mdzikolo.

A Trump alengeza izi pomwe khoti lina ku San Francisco mdzikolo layimitsa kaye ganizo lawo ndipo ati boma lawo lipambana pa ntchitoyo.

Pakadali pano sizikudziwika kuti chisinthe ndi chani pa lamulo latsopanolo.

Lachinayi lapitali khoti mdzikolo lidati boma la a Trump silikufotokoza mfundo zogwira mtima zoletsa nzika za chisilamu zina kulowa mdzikolo.

A Donald Trump akufuna kuti anthu a mayiko ena achisilamu asanu ndi awiri asamalowe mdziko la America-lo ngati mbali imodzi  yoteteza nzika za m’dziko la America ku anthu ochita za mtopola.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>