Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu kuti azikhala okondwera nthawi zonse mu chikondi cha Mulungu.
Papa amalankhula izi lero ku likulu la mpingowu ku Vatican pa mkumano omwe amakhala nawo ndi anthu omwe amakayendera malowa.
Iye wati Mulungu analenga zonse ngati mphatso ya chikondi chake choncho amaitana aliyense kuti chaulele chimenechi chikhale chikondwelero cha moyo wake.
Pamenepa Papa wati aliyense akuyenera kukhala chida cha chiyembekezo kuti kunyada komwe kumakhalapo pakati pa anthu kukhale ngati kwa Mulungu yemwe alibe tsankho.