Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Achinyamata Azigwiritsa Bwino Ntchito Luso la Makono Pofalitsa Uthenga wa Mulungu

$
0
0

Achinyamata a bungwe la Young Christian Workers (YCW) mumpingo wa katolika  awalangiza kuti azigwiritsa  bwino ntchito maluso atsopano omwe akubwera mdziko muno  monga ma computer komanso internet pantchito yofalitsa mawu a Mulungukomanso kupezapo zinthu zokhuza maphunziro.

Bambo mfumu a parish ya Kadikira, Bambo Godferry Ntchera  anena izi  pa m`bindikiro watsiku limodzi  wa  achinyamata a YCW a dinale ya Limbe omwe unachitikira ku NantipwiriPastrol  Centre.

“Tikuwunikikira za utumiki wa achinyamata ngati mboni za Yesu Khristu m’masiku amakono ano. Cholinga ndi chakuti achinyamata ngakhale akumana ndi mavuto osiyanasiyana asafooke kapena kubwelera mmbuyo koma akhale ndi mtima opitiriza kutumikira. Iwowanso awathandize anzawo omwe sachita zachikhristu kuti atembenuke mtima ayambenso nawo kukhala mboni za Yesu Khristu chifukwa achinyamatawa ndi mchere komanso kuwala kowalira ena amene ali mu mdima,” anatero bamboo Ntchera.

Iwo ati achinyamata akusokonekera  kamba koti akumaonera zinthu zolaula ndi makhalidwe olakwika zomwe pamapeto pake zikumasokoneza  moyo wawo wanthupi ndi wauzimu.

M`mawu ake wapampando wa bungwe la YCWmudinaleyi LenardMataka wati kudzera mu m`bindikirowu achinyamata alimbikitsidwa zomwe ziwathandize kuthana ndi mavuto omwe amakumana nawo tsiku ndi tsiku komanso kukhala nyale za ena.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>