Arkidayosizi ya mpingo wa katolika ya Blantyre yalimbikitsa akhristu a mpingowu kuti abzale mitengo ngati njira imodzi yobwezeretsa chilengedwe mdziko muno.
Vicar General wa arkidayosiziyi bambo Boniface Tamani alankhula izi pa mwambo wokhazikitsa ntchito yobzala mitengo yomwe ikutsogoleredwa ndi bungwe la amai achikatolika la Catholic Women Organization (CWO) mu arkidayosiziyi ndi thandizo la ndalama lochokera ku bank ya National.
Iwo ati ndi udindo wa mkhristu aliyense mogwirizana ndi atsogoleri a m’madera mwawo kudzala mitengo.
Mmawu ake mkulu woyang’anira ntchito za bank ya National a Austin Musyan ati apitiriza kuthandiza pa ntchito yobzala mitengo m’madera osiyanasiyana mdziko muno.
Mwa zina, mitengo yoposa 21 thousand ndi yomwe idzalidwe m’maparishi onse a mpingowu mu arkidayosiziyi ndipo ndi ya ndalama pafupifupi 3.5 million kwacha.