Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kulowa ma Bungwe Awiri a Nkhonya ndi Kuphwanya Malamulo-MPBCB

$
0
0

Bungwe lalikulu loyang’anira akatswiri omenya nkhonya mdziko muno la Malawi Professional Boxing Control Board lati ndi lokhumudwa kaamba ka mchitidwe wa omenya nkhonya ena omwe akugwira ntchito ndi mabungwe awiri osiyana zomwe ati ndi kuphwanya malamulo a masewerawa pa dziko lonse.

Mkulu wofalitsa nkhani ku bungweli a Frank Chibisa ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre.

Iwo ati malamulo a bungwe loyendetsa masewero a nkhonya  pa dziko lonse lapansi la World Boxing Council salola omenya nkhonya kukhala membala wa mabungwe awiri.

Izi zikudza potsatira kusamvana  komwe kwabuka pakati pa mabungwe awiri oyang’anira masewera a nkhonya a Malawi Professional Boxing Control Board ndi mamembala ena a bungwe la Malawi Boxing Association.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>