Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kuthetsa Matola Kwachepetsa Ngozi M’boma la Mangochi

$
0
0

Kuletsa kwa galimoto za matola m’boma la Mangochi ati kwathandiza kubweretsa bata pa nsewu komanso kuchepetsa ngozi za pansewu m’bomalo.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo inspector Rodrick Maida wauza Radio Maria Malawi kuti chikhazikitsireni ndondomeko  yoletsa galimoto za matola m’bomali, ndondomeko yomwe inakhazikitsidwa pa 20 November chaka chatha ndi akuluakulu a nthambi yoona za pansewu mdziko muno ya Road Traffic Directorate, madalaivala omwe akupezeka atanyamula anthu mu galimoto za lorry akumanjatidwa ndi kukaimbidwa mlandu woyika miyoyo ya anthu pa chiopsezo.

Padakali pano apolisiwa ati amanga komanso kulipilitsa chindapusa madalaivala a galimoto za mtundu wa lorry okwana khumi ndi awiri 12.

Anthuwa akagwidwa ati bwalo la milandu m’bomali likumawalamula kulipira chindapusa cha ndalama zoyambira 100 thousand kwacha mpaka 300 thousand kwacha kapena kulephera apo akakhale ku ndende.

Malamulowa akuloleza eni galimoto za mtundu wa lorry kunyamula katundu koma akuletsa kutengeramo anthu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>