Bambo wina wa zaka 49 zakubadwa wa mmudzi mwa Steven mdera la mfumu yaikulu Chowe m’boma la Mangochi wafa kaamba kodzimangilira mu mtengo.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Inspector Rodrick Maida wauza Radio Maria Malawi kuti malume ake a malemuyu a Liposa Lulanga anati malemuyu Sadiki Sumani wakhala akudwala kwa nthawi yaitali.
Pa chifukwa ichi malemuyu ati anapita ku chipatala cha Makumba kuti akalandire thandizo, ndipo ali kumene anaganiza zoyezetsa ngati ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi komwe anamupeza nako.
Inspector Maida ati pambuyo pomva zotsatirazi, malemuyu anasowa ndipo anthu a mmudzimo atamuyang’ana anakamupeza ku ntchire la mmudzilo atadzimangilira mu mtengo.
Malipoti a ku chipatala asonyeza kuti malemuyu wamwalira kaamba kodzikhweza.